37 Bezeri, ndi Hndi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.
38 Ndi ana a Yeteri: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.
39 Ndi ana a Ula: Ara, ndi Hanieli, ndi Rizya.
40 Awa onse ndiwo ana a Aseri, akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akuru mwa akalonga. Oyesedwa mwa cibadwidwe cao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi.