12 ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,
13 ndi abale ao, akuru a nyumba za makolo ao cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa Debito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu.
14 Ndi a Alevi: Semaya mwana wal Hasubu, mwana wa Azrikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari;
15 ndi Bakabakara, Heresi, ndi Galala, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;
16 ndi Obadiya mwana wa Semaya, mwana wa Galala, mwana wa Yedutuni, ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, wokhala m'midzi ya Anetofati.
17 Ndi odikira pakhomo: Salumu, ndi Akubu, ndi Talimoni, ndi Ahimani ndi abate ao; Salumu ndi mkuru wao,
18 amene adadikira pa cipata ca mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.