18 amene adadikira pa cipata ca mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.
19 Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiasafu; mwana wa Kora, ndi abale ace a nyumba ya atate wace; Akora anayang'anira nchito ya utumiki, osunga zipata za kacisi monga makolo ao; anakhala m'cigono ca Yehova osunga polowera;
20 ndi a Pinehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.
21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa cihema cokomanako.
22 Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa cibadwidwe cao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samueli mlauli anawaika m'udindo wao.
23 Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za ku nyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya kacisi, m'udikiro wao.
24 Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwela.