20 ndi a Pinehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.
21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa cihema cokomanako.
22 Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa cibadwidwe cao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samueli mlauli anawaika m'udindo wao.
23 Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za ku nyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya kacisi, m'udikiro wao.
24 Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwela.
25 Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao;
26 pakuti odikira anai akuru, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo cuma m'nyumba ya Mulungu.