1 NDIPO panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efraimu, dzina lace ndiye Elikana, mwana wace wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, M-efraimu.
2 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lace ndi Hana, mnzace dzina lace ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.
3 Ndipo munthuyu akakwera caka ndi caka kuturuka m'mudzi mwace kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Pinehasi.
4 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wace, ndi ana ace onse, amuna ndi akazi, gawo lao;
5 koma anapatsa Hana magawo awiri, cifukwa anakonda Hana, koma Mulungu anatseka mimba yace.
6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukuru, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yace.
7 Ndipo popeza munthuyo adatero caka ndi caka, popita mkaziyo ku nyumba ya Yehova, mnzaceyo amamputa; cifukwa cace iye analira misozi, nakana kudya.