6 Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.
7 Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.
8 Ndipo Jonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziu lula kwa iwo.
9 Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.
10 Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ici cidzatikhalira cizindikilo.
11 Ndipo onse awiri anadziulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikuturuka m'mauna m'mene anabisala.
12 Ndipo a ku kabomawo anayankha Jonatani ndi wonyamula zida zace, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Jonatani anauza wonyamula zida zace, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israyeli.