1 Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ace Aisrayeli; cifukwa cace tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.
2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera cimene Amaleki anacitira Israyeli, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kuturuka m'Aigupto.
3 Muka tsopano, nukanthe Amaleki, nuononge konse konse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamila ndi buru.
4 Ndipo Sauli anamemeza anthu, nawawerenga ku Telayimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.