1 Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Iwe ukuti ulire cifukwa ca Sauli nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israyeli? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ace.