14 Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akuru atatuwo anamtsata Sauli.
15 Koma Davide akamuka kwa Sauli, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wace ku Betelehemu.
16 Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.
17 Ndipo Jese anati kwa Davide mwana wace, Uwatengere abale ako efa watirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;
18 nunyamule ncinci izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa cikwi cao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire cikole cao,
19 Tsono Sauli, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israyeli, anali m'cigwa ca Ela, ku nkhondo ya Afilisti.
20 Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Jese; ndipo iye anafika ku linga la magareta, napeza khamu lirikuturuka kunka poponyanira nkhondo lirikupfuula.