29 Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?
30 Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.
31 Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Sauli; ndipo iye anamuitana.
32 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Asade nkhawa munthu ali yense cifukwa ca iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu.
33 Ndipo Sauli anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wace.
34 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina cimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo,
35 ndinacithamangira, ndi kucikantha, ndi kuiturutsa m'kamwa mwace; ndipo pamene cinaneliukira, ndinagwira cowa lace ndi kucikantha ndi kucipha.