39 Ndipo Davide anamanga lupanga lace pamwamba pa zobvala zace, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazibvula Davide.
40 Natenga ndodo yace m'dzanja lace nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo cibete; ndi coponyera miyala cinali m'dzanja lace, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.
41 Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.
42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.
43 Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.
44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.
45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza.