41 Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.
42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.
43 Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.
44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.
45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza.
46 Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukucotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu.
47 Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m'manja athu.