1 Ndipo Sauli analankhula kwa Jonatani mwana wace, ndi anyamata ace onse kuti amuphe Davide.
2 Koma Jonatani mwana wa Sauli anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Jonatani anauza Davide, nati, Sauli atate wanga alikufuna kukupha; cifukwa cace tsono ucenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale;
3 ndipo ine ndidzaturuka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.
4 Ndipo Jonatani analankhula ndi atate wace mobvomereza Davide, nanena naye, Mfumu asacimwire mnyamata wace Davide; cifukwa iyeyo sanacimwira inu, ndipo nchito zace anakucitirani zinali zabwino ndithu;
5 popeza iye anataya moyo wace nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anacitira Aisrayeli onse cipulumutso cacikuru, inu munaciona, nimnnakondwera; tsono mudzacimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda cifukwa?