13 Mulungu alange Jonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukucitira coipa, ine osakuululira, ndi kukucotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
14 Ndipo undionetsere cifundo ca Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;
15 komanso usaleke kucitira cifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse; mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Da vide pa dziko lapansi.
16 Comweco Jonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.
17 Ndipo Jonatani anamlumbiritsa Davide kaciwiri, cifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.
18 Tsono Jonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.
19 Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mrandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri.