4 Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.
5 Comweco Davide ndi anthu ace anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.
6 Ndipo kunali kuti Abyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lace.
7 Ndipo anthu anauza Sauli kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Sauli anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.
8 Ndipo Sauli anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ace.
9 Ndipo Davide anadziwa kuti Sauli analikulingalira zomcitira zoipa; nati kwa Abyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.
10 Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, mnyamata wanu wamva zoona kuti Sauli afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo cifukwa ca ine.