13 Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba pa phiri; pakati pao panati danga lalikuru;
14 ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abineri mwana wa Neri, nati, Suyankha kodi Abineri? Tsono Abineri anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?
15 Davide nati kwa Abineri, Si ndiwe mwamuna weni weni kodi? ndani mwa Aisrayeli afanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.
16 Ici unacicita siciri cabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, cifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi cikho ca madzi zinali kumutu kwace ziri kuti?
17 Ndipo Sauli anazindikira mau ace a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.
18 Nati iye, Cifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wace? pakuti ndacitanji? kapena m'dzanja langa muli coipa cotani?
19 Cifukwa cace mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wace. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire copereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipitikitsa lero kuti ndisalandireko colowa ca Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu yina.