13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.
14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.
15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ace anangokhala tong'o osapenya,
16 Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndacokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, a Nkhondoyo idatani, mwana wanga?
17 Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, lsrayeli anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukuru kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Pinehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandiwa.
18 Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa cambuyo pa mpando wace pam bali pa cipata, ndi khosi lace linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkuru thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israyeli zaka makumi anai.
19 Ndipo mpongozi wace, mkazi wa Pinehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yace yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wace, ndi mwamuna wace anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kucira kwace kwamdzera.