1 Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nacoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.
2 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo ku nyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.
3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa, taonani Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwace.
4 Ndipo m'mawa mwace polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wace ndi zikhato zonse ziwiri za manja ace zinagona zoduka paciundo; Dagoni anatsala thupi lokha.