4 Pomwepo ana a Israyeli anacotsa. Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.
5 Ndipo Samueli anati, Musonkhanitse Aisrayeli onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.
6 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lija, nati, Tinacimwira Yehova. Ndipo Samueli anaweruza ana a Israyeli m'Mizipa.
7 Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisrayeli anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisrayeli. Ndipo Aisrayeli pakumva ici, anacita mantha ndi Afilistiwo.
8 Ndipo ana a Israyeli anati kwa Samueli, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.
9 Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.
10 Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.