14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda yamphesa yanu, ndi minda yaazitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ace.
15 Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ace, ndi anyamata ace.
16 Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi aburu anu, nidzawagwiritsa nchito yace.
17 Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapoloace.
18 Ndipotsiku lija mudzapfuula cifukwa ca mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.
19 Koma anthu anakana kumvera mau a Samueli; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;
20 kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kuturuka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.