1 Ndipo panali munthu Mbenlamlni, dzina lace ndiye Kisi, mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.
2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lace Sauli, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israyeli panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'cifuwa.
3 Ndipo aburu a Kisi, atate wa Sauli, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Sauli mwana wace, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna aburuwo.
4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.