1 Caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Yoasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yoahazimwana wa Yehu analowa ufumu wace wa Israyeli ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.
2 Nacita coipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli; sanazileka.
3 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israyeli, nawapereka m'dzanja la Hazaeli mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli, masiku onsewoo
4 Koma Yoahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwace kwa Israyeli m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.
5 Ndipo Yehova anapatsa Israyeli mpulumutsi, naturuka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israyeli m'mahema mwao monga kale.
6 Komatu sanalekana nazo zolakwa za nyumba ya Yerobiamu, zimene analakwitsa nazo Israyeli, nayenda m'mwemo; nicitsalanso cifanizo m'Samariya.
7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyira Yoahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magareta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati pfumbi lopondapo.