22 Nagona Menahemu ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Pekahiya mwana wace.
23 Caka ca makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.
24 Nacita coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
25 Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wace, anamcitira ciwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobo ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya ku nyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Gileadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwace.
26 Macitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazicita, taonani zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
27 Caka ca makumi asanu mphambu ziwiri ca Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.
28 Nacita coipa pamaso pa Yehova: osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli,