1 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kabvumvulu, Eliya anacokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.
2 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndimke ku Beteli. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Beteli.
3 Ndipo ana a aneneri okhala ku Beteli anaturukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, lode ndidziwa, khalani muli cete.
4 Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.
5 Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli cete.