8 Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israyeli adang'amba zobvala zace, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zobvala zanu cifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israyeli.
9 M'mwemo: Namani anadza ndi akavalo ace ndi magareta ace, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.
10 Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.
11 Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.
12 Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israyeli? ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nacoka morunda.
13 Pamenepo anyamata ace anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani cinthu cacikuru, simukadacicita kodi? koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?
14 Potero anatsika, namira m'Yordano kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wace unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.