10 Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi aburu omanga, ndi mahema ali cimangire.
11 Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m'nyumba ya mfumu.
12 Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ace, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu aticitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, laturuka m'misasa, nabisala kuurengo, ndi kuti, Pamene aturuka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo.
13 Nayankha mmodzi wa anyamata ace, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsirizika; tiwatumize tione.
14 Motero anatenga magareta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.
15 Ndipo anawalondola mpaka ku Yordano; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zobvala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.
16 Naturuka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso wa ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.