3 Koma polowera pa cipata panali amuna anai akhate, nanenana wma ndi mnzace, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
4 Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.
5 Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.
6 Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magareta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikuru; nanenana wina ndi mnzace, Taonani mfumu ya Israyeli watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aaigupto, atigwere.
7 Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi aburu ao, misasa iri cimangire; nathawa, apulumutse moyo wao.
8 Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.
9 Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.