13 Tsono panali tsiku loti ana ace amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;
14 nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi aburu akazi analikudya pambali pao;
15 koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
16 Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wocokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
17 Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Akasidi anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamila, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
18 Akali cilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;
19 ndipo taonani, inadza mphepo yaikuru yocokera kucipululu, niomba pa ngondya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.