Yobu 27 BL92

Yobu adzikaniza nanenetsa kuti ocimwa ambiri akhala osalangidwa. Ena ali ndi nzeru ndi cuma, koma opanda nzeru yeni yeni

1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati,

2 Pali Mulungu, amene anandicotsera zoyenera ine,Ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,

3 Pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,Ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga;

4 Milomo yanga siilankhula cosalungama,Ndi lilime langa silichula zacinyengo.

5 Sindibvomereza konse kuti muli olungama;Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.

6 Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.

7 Mdani wanga akhale ngati woipa,Ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.

8 Pakuti ciyembekezo ca wonyoza Mulungu nciani pomlikhatu Mulungu,Pomcotsera moyo wace?

9 Kodi Mulungu adzamvera kupfuula kwace, ikamdzera nsautso?

10 Kodi adzadzikondweretsa naze Wamphamvuyonse,Ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?

11 Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;Cokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzacibisa.

12 Taonani, inu nonse munaciona;Ndipo mugwidwa nazo zopanda pace cifukwa ninji?

13 Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,Ndi colowa ca akupsinja anzao acilandira kwa Wamphamvtiyonse.

14 Akacuruka ana ace, ndiko kucurukira lupanga,Ndi ana ace sadzakhuta cakudya.

15 Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,Ndi akazi ace amasiye sadzalira maliro.

16 Cinkana akundika ndalama ngati pfumbi,Ndi kukonzeratu zobvala ngati dothi;

17 Azikonzeretu, koma wolungama adzazibvala,Ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.

18 Amanga nyumba yace ngati kadzoce,Ndi ngati wolindira amanga dindiro.

19 Agona pansi ali wacuma, koma saikidwa;Potsegula maso ace, wafa cikomo,

20 Zoopsa zimgwera ngati madzi;Nkuntho umtenga usiku.

21 Mphepo ya kum'mawa Imtenga, nacokaiye;Nimkankha acoke m'malo mwace.

22 Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osanlieka;Kuthawa akadathawa m'dzanja lace.