Yobu 11 BL92

Zofari adzudzula Yobu pa kudzilungamitsa kwace, namcenjeza alape

1 Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati,

2 Kodi mau ocurukawa sayenera kuwayankha?Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama?

3 Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa?Useka kodi, wopanda munthu wakukucititsapo manyazi?

4 Pakuti unena, Ciphunzitso canga ncoona,Ndipo ndiri woyera pamaso pako.

5 Koma, hal mwenzi atanena Mulungu,Ndi kukutsegulira milomo yace motsutsa;

6 Nakufotokozere zinsinsi za nzeru,Popeza zipindika-pindika macitidwe ao!Cifukwa cace dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.

7 Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?

8 Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungacitenji?Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?

9 Muyeso wace utalikira utali wace wa dziko lapansi,Citando cace ciposa ca nyanja.

10 Akapita, nakatsekera,Nakaturutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?

11 Pakuti adziwa anthu opanda pace,Napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira.

12 Koma munthu wopanda pace asowa nzeru,Ngakhale munthu abadwa ngati mwana wa mbidzi.

13 Ukakonzeratu mtima wako,Ndi kumtambasulira Iye manja ako;

14 Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uicotseretu kutali,Ndi cisalungamo cisakhale m'mahema mwako;

15 Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;Nudzalimbika osacita mantha;

16 Pakuti udzaiwala cisoni cako,Udzacikumbukila ngati madzi opita;

17 Ndipo moyo wako udzayera koposa usana;Kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa.

18 Ndipo udzalimbika mtima popeza pali ciyembekezo;Nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka,

19 Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa,Ndipo ambiri adzakupembedza,

20 Koma maso a oipa adzagoma, Ndi pothawirapo padzawasowa,Ndipo ciyembekezo cao ndico kupereka mzimu wao.