Yobu 8 BL92

Poona tsoka lao Bilidadi akuti Yobu ndi ana ace anacimwa, anena mofanizira

1 Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2 Udzanena izi kufikira liti?Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3 Ngati Mulungu akhotetsa ciweruzo?Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4 Cinkana ana ako anamcimwira Iye,Ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5 Koma ukafunitsitsa Mulungu,Ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6 Ukakhala woyera ndi woongoka mtima,Zoonadi adzakugalamukira tsopano,Ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7 Ndipo cinkana ciyambi cako cinali cacing'ono,Citsiriziro cako cidzacuruka kwambiri.

8 Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,Nusamalire zimene makolo ao adazisanthula;

9 Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,Popeza masiku athu a pa dziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10 Amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,Ndi kuturutsa mau a mumtima mwao?

11 Ngati gumbwa aphuka popanda cinyontho?Ngati mancedza amera popanda madzi?

12 Akali auwisi, sanawaceka,Auma, asanaume mathengo onse ena.

13 Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;Ndi ciyembekezo ca onyoza Mulungu cidzatayika;

14 Kulimbika mtima kwace kudzatyoka,Cikhulupiriro cace cikunga nyumba ya tandaude.

15 Adzatsamira nyumba yace, koma yosamlimbira;Adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16 Akhala wamuwisi pali dzuwa,Ndi nthambi zace ziturukira pamunda pace.

17 Mizu yace iyangayanga pa kasupe wamadzi,Apenyerera pokhalapo miyala.

18 Akamuononga kumcotsa pamalo pace,Padzamkana, ndi kuti, Sindinakuona.

19 Taona, ici ndico comkondweretsa panjira pace,Ndi panthaka padzamera ena.

20 Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;Kapena kugwiriziza ocita zoipa.

21 Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka,Ndi milomo yako kupfuula.

22 Iwo akudana nawe adzabvala manyazi;Ndi hema wa oipa adzakhala kuli zi.