1 Taonani; diso langa laciona conseci;M'khutu mwanga ndacimva ndi kucizindikira.
2 Cimene mucidziwa inu, inenso ndicidziwa;Sindikuceperani.
3 Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse,Ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu.
4 Koma inu ndinu opanga zabodza,Asing'anga opanda pace inu nonse.
5 Mwenzi mutakhala cete konse,Ndiko kukadakhala nzeru zanu.
6 Tamvani tsono kudzikanira kwanga,Tamverani kudzinenera kwa milomo yanga.
7 Kodi munenera Mulungu mosalungama,Ndi kumnenera Iye monyenga?
8 Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye?Mundilimbirana mwa Mulungu.
9 Ncokoma kodi kuti Iye akusanthuleni?Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?
10 Adzakudzudzulani ndithu,Mukacita tsankhu m'tseri.
11 Ukulu wace sukucititsani mantha,Ndi kuopsa kwace sikukugwerani kodi?
12 Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;Zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.
13 Khalani cete, ndilekeni, kuti ndinene,Condifikira cifike.
14 Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,Ndi kupereka moyo wanga m'dzanja langa?
15 Angakhale andipha koma ndidzamlindira;Komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pace.
16 Iye adzakhalanso cipulumutso canga,Pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pace.
17 Mvetsetsani mau anga,Ndi kunenetsa kwanga kumveke m'makutu mwanu.
18 Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;Ndidziwa kuti adzandimasula ndiri wolungama,
19 Ndaniyo adzatsutsana nane?Ndikakhala cete, ndidzapereka mzimu wanga.
20 Zinthu ziwiri zokha musandicitire,Pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu:
21 Mundicotsere dzanja lanu kutali,Ndi kuopsa kwanu kusandicititse mantha.
22 Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha;Kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu.
23 Mphulupulu zanga ndi zocimwa zanga ndi zingati?Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi cimo langa,
24 Mubisiranji nkhope yanu,Ndi kundiyesa mdani wanu?
25 Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,Ndi kulondola ziputu zouma?
26 Pakuti mundilembera zinthu zowawa,Ndi kundipatsa ngati colowa mphulupulu za ubwana wanga.
27 Mulonganso mapazi anga m'zigologolo, ndi kupenyerera mayendedwe anga onse;Mudzilembera malire mopanika mapazi anga;
28 Momwemo munthu akutha ngati cinthu coola,Ngati cobvala codyedwa ndi numbi