Yobu 31 BL92

1 Ndinapangana ndi maso anga,Potero ndipenyerenji namwali?

2 Pakuti gawo la Mulungu locokera kumwamba,Ndi colowa ca Wamphamvuyonse cocokera m'mwambamo nciani?

3 Si ndizo cionongeko ca wosalungama,Ndi tsoka la ocita mphulupulu?

4 Nanga sapenyanjira zanga,Ndi kuwerenga moponda mwanga monse?

5 Ngati ndinayanjana nalo bodza,Ndi phazi langa linathamangira cinyengo;

6 Andiyese ndi muyeso wolingana,Kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.

7 Ngati phazi langa linapambuka m'njira,Ndi mtima wanga unatsata maso anga?Ngati cirema camamatira manja anga?

8 Ndibzale ine nadye wina,Ndi zondimerera ine zizulidwe.

9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,Ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,

10 Mkazi wanga aperere wina;Wina namuike kumbuyo.

11 Pakuti ico ndi coipitsitsa,Ndico mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wace.

12 Pakuti ndico moto wakunyeka mpaka cionongeko,Ndi cakuzula zipatso zanga zonse.

13 Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga,Potsutsana nane iwo,

14 Ndidzatani ponyamuka Mulungu?Ndipo pondizonda Iye ndidzamyankha ciani?

15 Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenga iyenso?Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?

16 Ngati ndakaniza aumphawi cifuniro cao,Kapena kutopetsa maso a amasiye,

17 Kapena kudya nthongo yanga ndekha,Osadyako mwana wamasiye;

18 (Pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate;Ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye cibadwire ine.)

19 Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda cobvala,Kapena kuti wosowa alibe copfunda;

20 Ngati zuuno zace sizinandiyamika,Ngati sanapfunda ubweya wa nkhosa zanga;

21 Ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,Popeza ndinaona thandizo langa kucipata;

22 Libanthuke phewa langa paphalo,Ndi dzanja langa liduke pagwangwa.

23 Pakuti tsoka locokera kwa Mulungu linandiopsa,Ndi cifukwa ca ukulu wace sindinakhoza kanthu,

24 Ngati ndayesa golidi ciyembekezo canga,Ndi kunena ndi golidi woyengetsa,Ndiwe cikhazikitso canga;

25 Ngati ndinakondwera popeza cuma canga ncacikuru,Ndi dzanja langa lapeza zocuruka;

26 Ngati ndalambira dzuwa lirikuwala,Kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;

27 Ndi mtima wanga wakopeka m'tseri,Ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;

28 Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace;Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.

29 Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,Kapena kudzitukula pompeza coipa;

30 Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe,Kupempha motemberera moyo wace.

31 Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

32 Mlendo sakagona pakhwalala,Koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.

33 Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,Ndi kubisa mphulupulu yanga m'cifuwa mwanga;

34 Popeza ndinaopa unyinji waukuru,Ndi cipepulo ca mapfuko cinandiopsetsa;Potero ndinakhala cete osaturuka pakhomo panga.

35 Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera,Cizindikilo canga sici, Wamphamvuyonse andiyankhe;Mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wangal

36 Ndithu ndikadawasenza paphewa panga,Ndi kudzimangirira awa ngati korona.

37 Ndikadamfotokozera ciwerengo ca mopondamo mwanga,Ndikadamsenderera Iye ngati ka longa,

38 Ngati minda yanga ipfuula monditsutsa,Ndi nthumbira zace zilira pamodzi;

39 Ngati ndadya zipatso zace wopanda ndarama,Kapena kutayitsa eni ace moyo wao;

40 Imere minga m'malo mwa tirigu,Ndi dawi m'malo mwa barele.Mau a Yobu atha.