Yobu 36 BL92

Elihu alemekeza cilungamo ndi mphamvu ya Mulungu. Mulungu ndi wangwiro, ife tilephera kumdziwa

1 Elihu nabwereza, nati,

2 Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani,Pakuti ndiri naonso mau akunenera Mulungu.

3 Ndidzatenga nzeru zanga kutali,Ndidzabvomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.

4 Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza,Wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.

5 Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu;Mphamvu ya nzeru zace ndi yaikuru.

6 Sasunga woipa akhale ndi moyo,Koma awaninkha ozunzikazowayenera iwo.

7 Sawacotsera wolungama maso ace,Koma pamodzi ndi mafumu pa mpando waoAwakhazika cikhazikire, ndipo akwezeka.

8 Ndipo akamangidwa m'nsinga,Nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,

9 Pamenepo awafotokozera nchito zao,Ndi zolakwa zao, kuti anacita modzikuza.

10 Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize,Nawauza abwerere kuleka mphulupulu.

11 Akamvera ndi kumtumikira,Adzatsiriza masiku ao modala,Ndi zaka zao mokondwera.

12 Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,Nadzatsirizika osadziwa kanthu.

13 Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,Akawamanga Iye, sapfuulira.

14 Iwowa akufa akali biriwiri,Ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.

15 Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwace,Nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.

16 Inde akadakukopani mucoke posaukira,Mulowe kucitando kopanda copsinja;Ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.

17 Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa,Zolingirirazo ndi ciweruzo zidzakugwiranibe,

18 Pakuti mucenjere, mkwiyo ungakunyengeni mucite mnyozo;Ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.

19 Cuma canu cidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika,Kapena mphamvu yanu yonse yolimba?

20 Musakhumbe usiku,Umene anthu alikhidwe m'malo mwao.

21 Cenjerani, musaluniike kumphulupulu;Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22 Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23 Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24 Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

25 Anthu onse azipenyerera,Anthu aziyang'anira kutali.

26 Taonani, Mulungu ndiye wamkuru, ndipo sitimdziwa;Ciwerengo ca zaka zace ncosasanthulika.

27 Pakuti akweza madontho a mvula,Akhetsa mvula ya m'nkhungu yace

28 Imene mitambo itsanulira,Nibvumbitsira anthu mocuruka.

29 Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo,Ndi kugunda kwa msasa wace?

30 Taonani, Iye ayala kuunika kwace pamenepo.Nabvundikira kunsi kwace kwa nyanja.

31 Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu.Apatsa cakudya cocuruka.

32 Akutidwa manja ace ndi mphezi,Nailamulira igwere pofunapo Iye.