Yobu 22 BL92

Elifazi amchulira Yobu zoipa zambiri, namuuza alape, Mulungu nadzamcitira cifundo

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Kodi munthu apindulira Mulungu?Koma wanzeru angodzipindulira yekha.

3 Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama?Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako?

4 Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu,Cifukwa ca kumuopa kwako?

5 Zoipa zako sizicuruka kodi?Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi?

6 Pakuti wamtenga cikole kwa mbale wako wopanda cifukwa,Ndi kubvula ausiwa zobvala zao.

7 Sunampatsa wolema madzi amwe,Ndi wanjala unammana cakudya.

8 Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lace;Ndi munthu wobvomerezeka, anakhala momwemo.

9 Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu,Ndi manja a ana amasiye anatyoledwa.

10 Cifukwa cace misampha ikuzinga.Ndi mantha akubvuta modzidzimutsa,

11 Kapena mdima kuti ungaone,Ndi madzi aunyinji akumiza.

12 Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali?Ndipo penyani kutalika kwace kwa nyenyezi, ziri m'talitali.

13 Ndipo ukuti, Adziwa ciani Mulungu?Aweruza kodi mwa mdima wa bii?

14 Mitambo ndiyo comphimba, kuti angaone;Ndipo amayenda pa thambo lakumwamba.

15 Udzasunga kodi njira yakale,Anaiponda anthu amphulupulu?

16 Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao,Cigumula cinakokolola kuzika kwao;

17 Amene anati kwa Mulungu, Ticokereni;Ndipo, Angaticitire ciani Wamphamvuyonse?

18 Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino;Koma uphungu wa oipa unditalikira.

19 Olungama aciona nakondwera; Ndi osalakwa awaseka pwepwete,

20 Ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa,Ndi zowatsalira, moto unazipsereza.

21 Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere;Ukatero zokoma zidzakudzera,

22 Landira tsono cilamulo pakamwa pace,Nuwasunge maneno ace mumtimamwako.

23 Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino;Ukacotsera cosalungama kutali kwa mahema ako.

24 Ndipo utaye cuma cako kupfumbi,Ndi golidi wa ku ofiri ku miyala ya kumitsinje.

25 Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala cuma cako,Ndi ndarama zako zofunika.

26 Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse,Ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

27 Udzampemphera ndipo adzakumvera;Nudzatsiriza zowinda zako.

28 Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe;Ndi kuunika kudzawala pa njira zako.

29 Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza;Ndipo adzapulumutsa wodzicepetsayo.

30 Adzamasula ngakhale woparamula,Inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.