Yobu 14 BL92

1 Munthu wobadwa ndi mkaziNgwa masiku owerengeka, nakhuta mabvuto,

2 Aturuka ngati duwa, nafota;Athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3 Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,Ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4 Adzaturutsa coyera m'cinthu codetsa ndani? nnena mmodzi yense.

5 Popeza masiku ace alembedwa, ciwerengo ca miyezi yace cikhala ndi Inu,Ndipo mwamlembera malire ace, kuti asapitirirepo iye;

6 Mumleke osamthira maso, kuti apumule,Kuti akondwere nalo tsiku lace monga wolembedwa nchito.

7 Pakuti akaulikha mtengo pali ciyembekezo kuti udzaphukanso,Ndi kuti nthambi yace yanthete siidzasowa.

8 Ngakhale muzu wace wakalamba m'nthaka,Ndi tsinde lace likufa pansi;

9 Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,Nudzaswa nthambi ngati womera.

10 Koma munthu akufa atacita liondeondeInde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti?

11 Madzi acoka m'nyanja,Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12 Momwemo munthu agona pansi, osaukanso;Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,Kapena kuutsidwa pa tulo tace.

13 Ha! mukadandibisa kumanda,Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14 Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,Mpaka kwafika kusandulika kwanga,

15 Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;Mukadakhumba nchito ya manja anu.

16 Koma tsopano muwerenga maponda mwanga;Kodi simuyang'anitsa cimo langa?

17 Colakwa canga caikidwa m'thumba lokomedwa cizindikilo;Ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18 Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;Ndi thanthwe lisunthika m'malo mwace;

19 Madzi anyenya miyala;Zosefukira zao zikokolola pfumbi la nthaka;Ndipo muononga ciyembekezo ca munthu.

20 Mumlaka cilakire, napita iye;Musintha nkhope yace, mumuuza acoke.

21 Ana ace aona ulemu osadziwa iye;Napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.

22 Koma thupi lace limuwawira yekha,Ndi mtima wace umliritsa yekha.