Yobu 2 BL92

1 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.

3 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, cinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda cifukwa.

4 Nayankha Satana, nati kwa Yehoya, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wace.

5 Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza pfupa lace ndi mnofu wace, ndipo adzakucitirani mwano pamaso panu.

6 Ndipo Yehova anati kwa Satana. Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wace wokha uuleke.

7 Naturuka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zironda zowawa, kuyambira ku phazi lace kufikira pakati pamutu pace.

8 Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'mapulusa.

9 Pamenepo mkazi wace ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? citira Mulungu mwano, ufe.

10 Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? pa ici conse Yobu sanacimwa ndi milomo yace.

Mabwenzi ace atatu adzaceza naye

11 Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za coipa ici conse cidamgwera, anadza, yense kucokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

12 Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwa, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense maraya ace, nawaza pfumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13 Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukuru ndithu.