Yobu 40 BL92

1 Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati,

2 Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?Wocita makani ndi Mulungu ayankhe.

3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,

4 Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?Ndigwira pakamwa.

5 Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;Inde kawiri, koma sindionjezanso.

6 Ndipo Yehova anamyankha Yobu m'kabvumvulu, nati,

7 Dzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndidzakufunsa, undidziwitse.

8 Cingakhale ciweruzo canga udzacityola kodi?Udzanditsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?

9 Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?

10 Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika,Nubvale ulemu ndi ulemerero.

11 Tsanulira mkwiyo wako wosefuka,Nupenyerere ali yense wodzikuza ndi kumcepetsa,

12 Upenyerere ali yense wodzikuza, numtsitse,Nupondereze oipa pomwe akhala.

13 Uwakwirire pamodzi m'pfumbi,Uzimange nkhope zao pobisika.

14 Pamenepo inenso ndidzakubvomereza,Kuti dzanja lako lako lamanja likupulumutsa.

15 Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe,Ikudya udzu ngati ng'ombe.

16 Tapenya tsono, mphamvu yace iri m'cuuno mwace,Ndi kulimbalimba kwace kuli m'mitsempha ya m'mimba yace.

17 Igwedeza mcira wace ngati mkungudza;Mitsempha ya ncafu zace ipotana.

18 Mafupa ace akunga misiwe yamkuwa;Ziwalo zace zikunga zitsulo zamphumphu,

19 Iyo ndiyo ciyambi ca macitidwe a Mulungu;Wakuilenga anaininkha lupanga lace.

20 Pakuti mapiri aiphukitsira cakudya,Kumene zisewera nyama zonse za kuthengo,

21 Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,Pobisala pabango ndi pathawale.

22 Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao,Misondodzi ya kumtsinje iizinga.

23 Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera;Ilimbika mtima, ngakhale Yordano atupa mpaka pakamwa pace,