Yobu 33 BL92

Elihu atsutsa Yobu pa kudzikuza kwace, nanenetsa kuti pomlanga munthu Mulungu ali naco cifukwa

1 Komatu, Yobu, mumvere maneno anga,Mucherere khutu mau anga.

2 Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga,Lilime langa lanena m'kamwa mwanga.

3 Maneno anga aulula ciongoko ca mtima wanga,Ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.

4 Mzimu wa Mulungu unandilenga,Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.

5 Ngati mukhoza, mundiyankhe;Mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke.

6 Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu;Inenso ndinaumbidwa ndi dothi,

7 Taonani, kuopsa kwanga simudzacita nako mantha;Ndi ici ndikusenzetsani sicidzakulemererani.

8 Zedi mwanena m'makutu mwanga,Ndinamvanso mau akunena kwanu, akuti,

9 Ndine woyera ine, wopanda kulakwa,Ndine wosaparamula, ndiribe mphulupulu.

10 Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo,Andiyesa mdani wace;

11 Amanga mapazi anga m'zigologolo,Ayang'anira poyenda ine ponse.

12 Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama;Pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.

13 Mutsutsana ndi Iye cifukwa ninji?Popeza pa zace zonse saulula cifukwa.

14 Pakuti Mulungu alankhula kamodzi,Kapena kawiri, koma anthu sasamalira.

15 M'kulota, m'masomphenya a usiku,Pakuwagwera anthu tulo tatikuru,Pogona mwacheru pakama,

16 Pamenepo atsegula makutu a anthu,Nakomera cizindikilo cilangizo cao;

17 Kuti acotse munthu ku cimene akadacita,Ndi kubisira munthu kudzikuza kwace;

18 Kuti amletse angaonongeke,Ndi moyo wace ungatayike ndi lupanga.

19 Alangidwanso ndi zowawa pakama pace,Ndi kulimbana kowawa kosapuma m'mafupa ace.

20 M'mwemo mtima wace ucita mseru ndi mkate,Ndi moyo wace pa cakudya colongosoka.

21 Mnofu wace udatha, kuti sungapenyeke;Ndi mafupa ace akusaoneka aturuka.

22 Inde wasendera kufupi ku manda,Ndi moyo wace kwa akuononga.

23 Akakhala kwa iye mthenga,Womasulira mau mmodzi mwa cikwi,Kuonetsera munthu comuyenera;

24 Pamenepo Mulungu amcitira cifundo, nati,Mlanditse, angatsikire kumanda,Ndampezera dipo.

25 Mnofu wace udzakhala se, woposa wa mwana;Adzabwerera ku masiku a ubwana wace.

26 Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima;M'mwemo aona nkhope yace mokondwera;Ndipo ambwezera munthu cilungamo cace.

27 Apenyerera anthu, ndi kuti,Ndinacimwa, ndaipsa coongokaco,Ndipo sindinapindula nako.

28 Koma anandiombola ndingatsikire kumanda,Ndi moyo wanga udzaona kuunika.

29 Taona, izi zonse azicita MulunguKawiri katatu ndi munthu,

30 Kumbweza angalowe kumanda,Kuti kuunika kwa moyo kumuwalire.

31 Cherani khutu, Yobu, mundimvere ine;Mukhale cete, ndipo ndidzanena ine.

32 Ngati muli nao mau mundiyankhe.Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.

33 Ngati mulibe mau, tamverani Ine;Mukhale cete, ndipo ndizakuphunzitsani nzeru.