Yobu 10 BL92

1 Mtima wanga ulema nao moyo wanga,Ndidzadzilolera kudandaula kwanga,Ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.

2 Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse;Mundidziwitse cifukwa ca kutsutsana nane.

3 Cikukomerani kodi kungosautsa,Kuti mupeputsa nchito yolemetsa manja anu,Ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?

4 Muli nao maso a thupi kodi?Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?

5 Masiku anu akunga masiku a munthu kodi,Zaka zanu zikunga masiku a munthu;

6 Kuti mufunsa mphulupulu yanga,Ndi kulondola coipa canga;

7 Cinkana mudziwa kuti sindiri woipa,Ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?

8 Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu,Koma mufuna kundiononga.

9 Mukumbukile kuti mwandiumba ngati dothi;Ndipo kodi mudzandibwezera kupfumbi?

10 Simunanditsanula kodi ngati mkaka,Ndi kundilimbitsa ngati mase?

11 Munandibveka khungu ndi mnofu,Ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha,

12 Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima,Ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.

13 Koma izi munazibisa mumtima mwamu;Ndidziwa kuti ici muli naco:

14 Ndikacimwa mundipenya;Ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.

15 Ndikakhala woipa, tsoka ine;Ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutuwanga;Ndadzazidwa ndi manyazi, Koma penyani kuzunzika kwanga.

16 Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango;Mubweranso ndi kudzionetsera modabwiza kwa ine.

17 Mundikonzeranso mboni zonditsutsa,Ndi kundicurukitsira mkwiyo wanu;Nkhondo yobwereza-bwereza yandigwera.

18 Potero munandibadwitsa cifukwa ninji?Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.

19 Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala;Akadanditenga pobadwapo kumka nane kumanda.

20 Masiku anga satsala owerengeka nanga? lindani,Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono,

21 Ndisanacoke kumka kumene sindikabweranso,Ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa;

22 Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani,Dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka,Kumene kuunika kukunga mdima.