Yobu 21 BL92

Yobu ayankha kuti oipa ambiri amalemerera. Zooneka m'maso sizitiuza za mtima wa Mulungu

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Mvetsetsani mau anga;Ndi ici cikhale citonthozo canu.

3 Mundilole, ndinene nanenso; Ndipo nditanena ine, sekani.

4 Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu?Ndipo ndilekerenji kupsa mtima?

5 Ndiyang'anireni, nimusumwe,Gwirani pakamwa panu.

6 Ndikangokumbukila ndibvutika mtima,Ndi thupi langa licita nyau nyau.

7 Oipa akhaliranji ndi moyo,Nakalamba, nalemera kwakukuru?

8 Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao,Ndi ana ao pamaso pao,

9 Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha,Ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.

10 Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika;Ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.

11 Aturutsa makanda ao ngati gulu,Ndi ana ao amabvinabvina.

12 Ayimbira lingaka ndi zeze,Nakondwera pomveka citoliro.

13 Atsekereza masiku ao ndi zokoma,Natsikira m'kamphindi kumanda.

14 Koma adati kwa Mulungu, Ticokereni;Pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.

15 Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire?Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?

16 Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao;(Koma uphungu wa oipa unditalikira.)

17 Ngati nyali za oipa zizimidwa kawiri kawiri?Ngati tsoka lao liwagwera?Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wace?

18 Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo,Ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?

19 Mukuti, Mulungu asungira ana ace a munthu coipa cace,Ambwezere munthuyo kuti acidziwe.

20 Aone yekha cionongeko cace m'maso mwace,Namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.

21 Pakuti comsamalitsa nyumba yace nciani, atapita iye,Ciwerengo ca miyezi yace citadulidwa pakati?

22 Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru?Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.

23 Wina akufa, wabiriwiri,Ali cikhalire ndi cipumulire.

24 Mbale zace zidzala ndi mkaka;Ndi wongo wa m'mafupa ace uli momwe.

25 Koma mnzace akufa ali nao mtima wakuwawa,Osalawa cokoma konse.

26 Iwo agona cimodzimodzi kupfumbi,Ndi mphutsi ziwakuta.

27 Taonani, ndidziwa maganizo anu,Ndi ciwembu mundilingirira moipa,

28 Pakuti munena, Iri kuti nyumba ya kalonga?Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?

29 Simunawafunsa kodi opita m'njira?Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?

30 Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka?Naturutsidwa tsiku la mkwiyo?

31 Adzamfotokozera ndani njira yace pamaso pace?Nadzamlipitsa ndani pa ici anacicita?

32 Potsiriza pace adzapita naye kumanda,Nadzadikira pamanda pace,

33 Zibuma za kucigwa zidzamkomera.Adzakoka anthu onse amtsate,Monga anamtsogolera osawerengeka.

34 Potero munditonthozeranji nazo zopanda pace,Popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha?