Yobu 6 BL92

Yobu akuti ali ndi cifukwa ca kudandaula, alira kufa, adzuzula mabwenzi pa kuuma mtima kwao, apempha Mulungu amcitire cifundo

1 Koma Yobu anayankha, nati,

2 Mwenzi atayesa bwino cisoni canga,Ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!

3 Pakuti zikadalemera tsopano koposa mcenga wa kunyanja;Cifukwa cace mau anga ndasonthokera kunena.

4 Pakuti mibvi ya Wamphamvuyonse yandilowa,Mzimu wanga uumwa ulembe wace;Zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.

5 Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu?Ilira kodi ng'ombe pa cakudya cace?

6 Kodi cinthu cosakolera cidyeka copanda mcere?Coyera ca dzira cikolera kodi?

7 Zimene moyo wanga ukana kuzikhudzaZikunga cakudya cosakolera kwa ine.

8 Ha! ndikadakhala naco cimene ndicipempha,Mulungu akadandipatsa cimene ndicilira!

9 Cimkomere Mulungu kundiphwanya,Alole dzanja lace lindilikhel

10 Pamenepo ndidzasangalala,Ndidzakondwera naco cowawa cosandileka;Pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.

11 Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?

12 Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?

13 Mulibe thandizo mwa ine ndekha; cipulumutso candithawa.

14 Iye amene akadakomoka, bwenzi lace ayenera kumcitira cifundo;Angaleke kuopa Wamphamvuyonse.

15 Abale anga anacita monyenga ngati kamtsinje,Ngati madzi a timitsinje akupitirira.

16 Amada cifukwa ca madzi oundana.M'menemo cipale cofewa cibisika;

17 Atafikira mafundi, mitsinje iuma;Kukatentha, imwerera m'malo mwao.

18 Aulendo akutsata njira yao apambukapo,Akwerera poti se, natayika.

19 Aulendo a ku Tema anapenyerera,Makamu a ku Seba anaiyembekezera.

20 Anazimidwa popeza adaikhulupirira;Anafikako, nathedwa nzeru.

21 Pakuti tsopano mukhala mamwemo;Muona coopsa, mucitapo mantha.

22 Ngati ndinati, Mundipatse?Kapena, Muperekeko kwa ine cuma canu?

23 Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani?Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa?

24 Mundilangize, ndipo ndidzakhala cete ine;Mundizindikiritse umo ndinalakwira.

25 Mau oongoka si ndiwo amphamvu?Koma kudzudzula kwanu mudzudzula ciani?

26 Kodi muyesa kudzudzula mau?Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.

27 Indetu, mugwetsera wamasiye msampha,Mumkumbira bwenzi lanu mbuna.

28 Koma tsopano balindani, mundipenyerere;Ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.

29 Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu;Inde, bwereraninso, mlandu wanga ngwolungama.

30 Kodi pali cosalungama palilime panga?Ngati sindizindikira zopanda pace m'kamwa mwanga?