Yobu 28 BL92

1 Koma kuli mtapo wa siliva, Ndi malo a golidi amene amuyenga.

2 Citsulo acitenga m'nthaka,Ndi mkuwa ausungunula kumwala.

3 Munthu athawitsa mdima,Nafunafuna mpaka malekezero onse,Miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.

4 Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;Aiwalika ndi phazi lopitapo;Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.

5 Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya,Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.

6 Miyala yace ndiyo malo a safiro,Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.

7 Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.

8 Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.

9 Munthu atambasulira dzanja lace kumwala;Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.

10 Asema njira pakati pa matanthwe,Ndi diso lace liona ciri conse ca mtengo wace.

11 Atseka mitsinje ingadonthe;Naturutsira poyera cobisikaci.

12 Koma nzeru, idzapezeka kuti?Ndi luntha, malo ace ali kuti?

13 Munthu sadziwa mtengo wace;Ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.

14 Pozama pakuti, Mwa ine mulibe;Ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.

15 Silipezeka ndi golidi,Sayesapo siliva mtengo wace.

16 Sailinganiza ndi golidi wa Ofiri,Ndi sohamu wa mtengo wace wapatali kapena safiro.

17 Golidi ndi krustalo sizilingana nayo;Ndi kusinthana kwace, siisinthanika ndi zisambiro za golidi woyengetsa.

18 Korali kapena ngale sizikumbukikapo.Mtengo wace wa nzeru uposa wa korali wofiira.

19 Topazi wa Kusi sufanana nayo,Sailinganiza ndi golidi wolongosoka.

20 Koma nzeru ifuma kuti?Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?

21 Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,

22 Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.

23 Mulungu ndiye: azindikira njira yace,Ndiye adziwa pokhala pace.

24 Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,Naona pansi pa thambo ponse;

25 Pamene anaikira mphepo muyeso wace,Nayesera madzi miyeso;

26 Pakucitira mvula lamulo,Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;

27 Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;Anaikonza, naisanthula.

28 Koma kwa munthu anati,Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.