Yobu 9 BL92

Yobu abvomereza ukulu wa Mulungu, koma okoma ndi oipa alangidwa mmodzimodzi. Masautso ace amfunitsa kufa

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Zoona, ndidziwa kuti ciri cotero.Koma munthu adzakhala walungama bwanji kwa Mulungu?

3 Akafuna Iye kutsutsana naye,Sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa cikwi.

4 Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikuru;Ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

5 Ndiye amene asuntha mapiri, osacidziwa iwo,Amene amagubuduza mu mkwiyo wace.

6 Amene agwedeza dziko lapansi licoke m'malo mwace,Ndi mizati yace injenjemere.

7 Amene alamulira dzuwa ndipo silituruka,Nakomera nyenyezi cizindikilo cakuzitsekera.

8 Woyala thambo yekha,Naponda pa mafunde a panyanja.

9 Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe,Ndi Kumpotosimpita,

10 Wocita zazikuru zosasanthulika,Ndi zodabwiza zosawerengeka,

11 Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;Napitirira, koma osamaindikira ine.

12 Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?Adzanena naye ndani, Mulikucita ciani?

13 Mulungu sadzabweza mkwiyo wace;Athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.

14 Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji,Ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?

15 Ameneyo, cinkana ndikadakhala wolungama, sindikadamyankha; Ndikadangompembedza wondiweruza ine.

16 Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye,Koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga,

17 Pakuti andityola ndi mkuntho,Nacurukitsa mabala anga kopanda cifukwa.

18 Sandilola kuti ndipume,Koma andidzaza ndi zowawa.

19 Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu?Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?

20 Cinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa;Cinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu.

21 Cinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini,Ndipeputsa moyo wanga.

22 Kuli cimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikutiIye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.

23 Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,Adzaseka tsoka la wosacimwa.

24 Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa;Aphimba maso a oweruza ace.Ngati sindiye, pali yaninso?

25 Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;Athawa osaona cokoma.

26 Apitirira ngati zombo zaliwiro;Ngati mphungu igudukira cakudya cace.

27 Ndikati, Ndidzaiwala condidandaulitsa,Ndidzasintha nkhope yanga yacisoni, ndidzasekerera;

28 Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,Ndidziwa kuti simudzandiyesa wosacimwa.

29 Mlandu udzanditsutsa;Potero ndigwire nchito cabe cifukwa ninji?

30 Ndikasamba madzi a cipale cofewaNdi kuyeretsa manja anga ndi sopo;

31 Mudzandibviikanso muli zoola,Ndi zobvala zanga zidzanyansidwa nane.

32 Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe,Kuti tikomane mlandu.

33 Palibe wakutiweruza,Wakutisanjika ife tonse awiri manja ace.

34 Andicotsere ndodo yace,Coopsa cace cisandicititse mantha;

35 Kuti ndinene, osamuopa,Pakuti sinditero monga umo ndiri.