Yobu 29 BL92

Yobu alinganiza cikhalidwe cace cakale ndi tsoka latsopano, nalimbika kuti sanacita zochulidwazi

1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati,

2 Ha! ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi,Monga m'masiku akundisunga Mulungu;

3 Muja nyali yace inawala pamutu panga,Ndipo ndi kuunika kwace ndinayenda mumdima;

4 Monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba,Muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga;

5 Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi,Ndi ana anga anandizinga;

6 Muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka,Ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta aazitona!

7 Muja ndinaturuka kumka kucipata kumudzi,Muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,

8 Anyamata anandiona nabisala,Okalamba anandinyamukira, nakhala ciriri,

9 Akalonga anadziletsa kulankhula,Ndi kugwira pakamwa pao;

10 Mau a omveka anali zi,Ndi lilime lao linamamatira ku malakalaka ao.

11 Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa;Ndipo pondiona diso, linandicitira umboni.

12 Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakupfuula;Mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.

13 Dalitso la iye akati atayike linandidzera,Ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauyimbitsa mokondwera.

14 Ndinabvala cilungamo, ndipo cinandibvala ine;Ciweruzo canga cinanga mwinjiro ndi nduwira.

15 Ndinali maso a akhungu,Ndi mapazi a otsimphina.

16 Ndinali atate wa waumphawi;Ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa.

17 Ndipo ndinatyola nsagwada ya wosalungama,Ndi kukwatula cogwidwa kumano kwace.

18 Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'cisa canga;Ndipo ndidzacurukitsa masiku anga ngati mcenga.

19 Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;Ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.

20 Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,Ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga.

21 Anthu anandimvera, nalindira,Nakhala cete, kuti ndiwapangire.

22 Nditanena mau anga sanalankhulanso,Ndi kunena kwanga kunawakhera.

23 Anandilindira ngati kulindira mvula,Nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.

24 Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;Ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.