Yobu 3 BL92

Madandaulo a Yobu

1 Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pace, natemberera tsiku lace.

2 Nalankhula Yobu nati,

3 Litayike tsiku lobadwa ine,Ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.

4 Tsiku lija likhale mdima;Mulungu asalifunse kumwamba,Ndi kuunika kusaliwalire.

5 Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese lao lao;Mtambo ulikhalire;Zonse zodetsa usana bi ziliopse.

6 Usiku uja, mdima weni weni uugwere;Usakondwerere mwa masiku a m'caka;Usalowe m'ciwerengedwe ca miyezi.

7 Ha! usiku uja ukhale cumba;Kuyimbira kokondwera kusalowem'mwemo.

8 Autemberere iwo akutemberera usana,Odziwa kuutsa cinjokaco.

9 Nyenyezi za cizirezire zide;Uyembekezere kuunika, koma kuusowe;Usaone kuphenyuka kwa mbanda kuca;

10 Popeza sunatseka pa makomo ace mimba ya mai wanga.Kapena kundibisira mabvuto pamaso panga.

11 Ndinalekeranji kufera m'mimba?Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine?

12 Anandilandiriranji maondo?Kapena mabere kuti ndiyamwe?

13 Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala cete;Ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;

14 Pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,Akudzimangira m'mabwinja;

15 Kapena pamodzi ndi akalonga eni ace a golidi,Odzaza nyumba zao ndi siliva;

16 Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zi;Ngati makanda osaona kuunika.

17 Apo oipa aleka kumabvuta;Ndi apo ofoka mphamvu akhala m'kupumula.

18 Apo a m'kaidi apumula pamodzi,Osamva mau a wofulumiza wao.

19 Ang'ono ndi akulu ali komwe;Ndi kapolo amasuka kwa mbuyace.

20 Amninkhiranji kuunika wobvutika,Ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

21 Wakuyembekezera imfa, koma kuli zi,Ndi kuikumba koposa cuma cobisika,

22 Wakusekerera ndi cimwemweNdi kukondwera pakupeza manda?

23 Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika,Amene wamtsekera Mulungu?

24 Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga;Ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi.

25 Pakuti cimene ndinaciopa candigwera,Ndi cimene ndacita naco mantha candidzera.

26 Wosakhazikika, ndi wosakhala cete, ndi wosapumula ine,Koma mabvuto anandidzera.