1 Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pace pa iye mwini.
2 Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi, wa cibale ca Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.
3 Adapsa mtima pa mabwenzi ace atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.
4 Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.
5 Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.
6 Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati,Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.
7 Ndinati, Amisinkhu anene,Ndi a zaka zocuruka alangize nzeru.
8 Koma m'munthu muli mzimu,Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.
9 Akulu sindiwo eni nzeru,Ndi okalamba sindiwo ozindikira ciweruzo.
10 Cifukwa cace ndinati, Ndimvereni ine,Inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.
11 Taonani, ndinalindira mau anu,Ndinacherera khutu zifukwa zanu,Pofunafuna inu ponena.
12 Inde ndinasamalira inu;Koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu,Kapena wakumbwezera mau pakati painu.
13 Msamati, Tapeza nzeru ndife,Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;
14 Popeza sanandiponyera ine mau,Sindidzamyankha ndi maneno anu.
15 Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau.
16 Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo,Popeza akhala du osayankhanso?
17 Ndidzayankha inenso mau anga,Ndidzaonetsa inenso za m'mtima mwanga.
18 Pakuti ndadzazidwa ndi mau,Ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.
19 Taonani, m'cifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira,Ngati matumba atsopano akuti aphulike.
20 Ndidzanena kuti cifundo citsike;Ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha.
21 Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu,Kapena kumchula munthu maina omdyola nao;
22 Pakuti sindidziwa kuchula maina osyasyalika;Ndikatero Mlengi wanga adzandicotsa msanga.