1 Koma Yobu anayankha, nati,
2 Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti,Ndi kundityolatyola nao mau?
3 Kakumi aka mwandicititsa manyazi;Mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.
4 Ndipo ngati ndalakwa ndithu,Kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.
5 Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;
6 Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.
7 Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.
8 Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.
9 Anandibvula ulemerero wanga,Nandicotsera korona pamutu panga,
10 Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;Nacizula ciyembekezo canga ngati mtengo.
11 Wandiyatsiranso mkwiyo wace,Nandiyesera ngati wina wa adani ace.
12 Ankhondo ace andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,Nandimangira misasa pozinga hema wanga.
13 Iye anandicotsera abale anga kutali,Ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.
14 Anansi anga andisowa,Ndi odziwana nane bwino andiiwala.
15 Iwo a m'nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo;Ndine wacilendo pamaso pao.
16 Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau,Cinkana ndimpembedza pakamwa panga.
17 Mpweya wanga unyansira mkazi wanga,Cinkana ndinampembedza ndi kuchula ana a thupi langa.
18 Angakhale ana ang'ono andipeputsa,Ndikanyamuka, andinena;
19 Mabwenzi anga eni eni onse anyansidwa nane;Ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.
20 Pfupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga,Ndipo ndapulumuka ndiri nazo nkhama za mano anga.
21 Ndicitireni cifundo, ndicitireni cifundo, mabwenzi anga inu;Pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.
22 Mundilondola bwanji ngati Mulungu,Losakukwanirani thupi langa?
23 Ha! akadalembedwa mau anga!Ha! akadalembedwa m'buku!
24 Akadawazokota pathanthwe cikhalire,Ndi cozokotera cacitsulo ndi kuthira ntobvu!
25 Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo,Nadzauka potsiriza papfumbi.
26 Ndipo khungu langa litaonongeka,Pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu;
27 Amene ndidzampenya ndekha,Ndi maso anga adzamuona, si wina ai.Imso zanga zatha m'kati mwanga.
28 Mukati, Tiyeni timlondole!Popeza cifukwa ca mlandu capezeka mwa ine;
29 Mucite nalo mantha lupanga; Pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga,Kuti mudziwe pali ciweruzo.