Yobu 16 BL92

Yobu atonza mabwenziwo kuti mau ao samthandiza, akana kuti sanacimwa, nadziponya kwa Mulungu. Ciyembekezo cace ndi imfa

1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2 Ndamva zambiri zotere;Inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa.

3 Kodi adzatha mau ouluzika?Kapena cikuwindula nciani kuti uyankha zotere?

4 Inenso ndikadanena monga inu,Moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga,Ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu,Ndi kukupukusirani mutu wanga.

5 Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga,Ndi citonthozo ca milomo yanga cikadatsitsa cisoni canu.

6 Cinkana ndinena cisoni canga sicitsika;Ndipo ndikaleka, cindicokera nciani?

7 Koma tsopano wandilemetsa Iye;Mwapasula msonkhano wanga wonse.

8 Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa,Kuonda kwanga kundiukira, kucita umboni pamaso panga.

9 Iye ananding'amba m'kundida kwace, nakwiya nane,Anandikukutira mano;Mdani wanga ananditong'olera maso ace.

10 Iwo anandiyasamira pakamwa pao;Anandiomba pama ndi kunditonza;Asonkhana pamodzi kunditsutsa.

11 Mulungu andipereka kwa osalungama,Nandiponya m'manja a oipa.

12 Ndinali mkupuma, koma anandityola;Inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya;Anandiimika ndikhale candamali.

13 Eni mauta ace andizinga,Ang'amba imso zanga, osazileka;Natsanulira pansi ndulu yanga.

14 Andipasula-pasula;Andithamangira ngati wamphamvu.

15 Ndadzisokerera ciguduli ku khungu langa,Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'pfumbi.

16 Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi,Ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;

17 Pangakhale palibe ciwawa m'manja mwanga,Ndi pemphero langa ndi loyera.

18 Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga,Ndi kulira kwanga kusowe popumira.

19 Tsopanonso, taona, mboni yanga iri kumwamba,Ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba.

20 Mabwenzi anga andinyoza; Koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu;

21 Ha! munthu akadapembedzera mnzace kwa Mulungu,Monga munthu apembedzera mnansi wace!

22 Pakuti zitafika zaka zowerengeka,Ndidzamuka ku njira imene sindibwererako.