1 Pamenepo anayankha Zofari Mnaama, nati,
2 M'mwemo zolingirira zanga zindiyankha,Cifukwa cace ndifulumidwa m'kati mwanga.
3 Ndamva kudzudzula kwakundicititsa manyazi,Ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha.
4 Kodi sucidziwa ici ciyambire kale lomwe,Kuyambira anaika munthu pa dziko lapansi,
5 Kuti kupfuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha,Ndi cimwemwe ca wonyoza Mulungu cikhala kamphindi?
6 Cinkana ukulu wace ukwera kumka kuthambo,Nugunda pamitambo mutu wace;
7 Koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zace;Iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?
8 Adzauluka ngati loto, osapezekanso;Nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.
9 Diso lidamuonalo silidzamuonanso;Ndi malo ace sadzampenyanso.
10 Ana ace adzapempha aumphawi awakomere mtima;Ndi manja ace adzabweza cuma cace.
11 Mafupa ace adzala nao unyamata wace,Koma udzagona naye pansi m'pfumbi.
12 Cinkana coipa cizuna m'kamwa mwace,Cinkana acibisa pansi pa lilime lace;
13 Cinkana acisunga, osacileka,Naoikhalitsa m'kamwa mwace;
14 Koma cakudya cace cidzasandulika m'matumbo mwace,Cidzakhala ndulu ya mphiri mkati mwace.
15 Anacimeza cuma koma adzacisanzanso;Mulungu adzaciturutsa m'mimba mwace.
16 Adzayamwa ndulu ya mphiri;Pakamwa pa njoka padzamupha.
17 Sadzapenyerera timitsinje,Toyenda nao uci ndi mafuta.
18 Cimene adagwiriraco nchito, adzacibweza, osacimeza;Sadzakondwera monga mwa zolemera zace adaziona.
19 Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi;Analanda nyumba mwaciwawa, imene sanaimanga.
20 Popeza sanadziwa kupumula m'kati mwace,Sadzalanditsa kanthu ka zofunika zace.
21 Sikunatsalira kanthu kosadya iye,Cifukwa cace zokoma zace sizidzakhalitsa.
22 Pomkwanira kudzala kwace adzakhala m'kusauka;Dzanja la yense wobvutika lidzamgwera,
23 Poti adzaze mimba yace,Mulungu adzamponyera mkwiyo wace waukali,Nadzambvumbitsira uwu pakudya iye.
24 Adzathawa cida cacitsulo,Ndi mubvi wa uta wamkuwa udzampyoza.
25 Auzula, nuturuka m'thupi mwace;Inde nsonga yonyezimira ituruka m'ndulu mwace;Zamgwera zoopsa.
26 Zamdima zonse zimsungikira zikhale cuma cace,Moto wosaukoleza munthu udzampsereza;Udzatha wotsalira m'hema mwace.
27 M'mwamba mudzabvumbulutsa mphulupulu yace,Ndi dziko lapansi lidzamuukira.
28 Phindu la m'nyumba mwace lidzacoka,Akatundu ace adzamthawa tsiku la mkwiyo wace.
29 Ili ndi gawo la munthu woipa, locokera kwa Mulungu,Ndi colowa amuikiratu Mulungu.